His Majesty Kalonga Sosola IX News Flash with Snr Chief Dr Kaomba Refuting Fake News 06 05 2026 #ix
Mankhamba City
0:00 / 0:00
His Majesty Kalonga Sosola IX News Flash with Snr Chief Dr Kaomba Refuting Fake News 06 05 2026 #ix
972 просмотра · 5 мес. назад
Mankhamba City
947 подписчиков
972 просмотра · 5 мес. назад
#newsflash #BREAKING #NEWS
DZUKA MCHEWA DZUKA
LERO PA 07 MAY 2026
Ulemu kwa His Majesty Kalonga Sosola #IX, a patron ndi achiwiri awo, Chiefs Council, Mafumu onse ndi atsogoleri onse a MaCHE. Pomaliza Ulemu kwa achewa ndi malawi onse.
KUTSUTSA ZOMWE WALANKHULA BAMBO EMMANUEL SUNGANIMOYO.
His Majesty Kalonga Sosola #IX akuuza mtundu wachichewa onse kuti dzulo sichidali chikonzekero chake cholankhula ku mtundu ndi dziko la Malawi. Izi adachita pofuna kutsutsa msanga bodza lamkunkhuniza limene bambo Sunganimoyo wanena mukanema yao pa WhatsApp dzulo liriwisiri.
His Majesty Kalonga Sosola #IX pamodzi ndi SC. Dr. Kaomba akana mwamtuwagalu za kuti awiriwa akanganukana.
SC Dr. Kaomba ati iwo sadasemphane China chirichonse ndi His Majesty Kalonga Sosola #IX ayi. Ndipo sizingatheke zomwe bambo Sunganimoyo akulengeza. Iye akukhupirira kuti bambo Sunganimoyo ali pachintchito chachikulu chofuna kuti anthu aziberedwabe chuma ndi chikhalidwe cha pomapita kwa Gawa Undi ku Zambia
His Majesty Kalonga Sosola #IX ndi SC. Dr Kaomba pali ubale ndi mgwirizano waukulu pakati pao kuchokera ku ufumu ndi kubanja la Kalonga.
Kalonga Sosola #IX akutsimikizira mtundu ndi dziko la Malawi kuti asamvere akanyembete otere. Izi ndi Mbava zobwera mtundu wachichewa,
Kalonga Sosolayo watinso achewa tonse tikhala tikukumana ndi ndiphsyi zoterezi kufikira ufumu wake utatambalala dziko lonse monga makolo ake ankalamulira.
Iye akuchenjeza bambo Sunganimoyo kuti akuyenera kukhala ndi manyazi pofuna kupitiriza kumasokoneza ndi kubera achewa ndi boma la Malawi.
Pomaliza His Majesty Kalonga Sosola IX a kulimbikitsa umodzi ndi chitukuko pakati pa mtundu wa chichewa. Iye wapemphaso mafumu ndi achewa tonse kuti asataye mtima kapena kukhumudwa pamene azikumana kawirikawiri ndi anthu osafunira zabwino mtundu wao omwe.
wapempha Mafumu, boma ndi achewa onse kuti asasonkhe ndalama kapena chuma China chirichonse katundu wina aliyense kupititsa ku Zambia ku Mkaika. Iye wanenetsa kuti ubale wake ndi Gawa Undi mulibwino monga momwe makolo awo adawasiyira. Sibwino kumalimbikitsa maphokoso ku chichewa.
Ine
Potiphar Benson Banda
(Mneneri wa Kalonga ndi Chifukwato Cha Achewa)