Rodwell Lumbe Nzika Citizen Real Estate Ali pa Wanted panopa wathawa sakuonekaso
Malawian Cameras
0:00 / 0:00
Rodwell Lumbe Nzika Citizen Real Estate Ali pa Wanted panopa wathawa sakuonekaso
4 864 просмотра · 8 часов назад
Malawian Cameras
113 тыс. подписчиков
4 864 просмотра · 8 часов назад
Anthu pafupifupi 25 akufunafuna mwini wake wa kampani yogulitsa malo (Citizen Real Estate Company) a Rodwell Lumbe atawatengera ndalama zawo kuti awapatsa malo.
Oyankhulira makasitomala omwe anagula malo ku kampaniyi, a Rodrick Kuwani ati a Lumbe anagulitsa malo anthuwa ku Nathenje mu mzinda wa Lilongwe pa mitengo yosiyanasiyana.
Mwa chitsanzo, iwo analipira ndalama zokwana K17.5 million kuti atenga malo awo anthu akakolola popeza pa nthawiyo anthu anali asanakolole mbewu zawo.
A Kuwani ati nthawi itakwana yotenga malo awo, a Lumbe anayamba kuthawathawa, samayankha lamya yawo ya m'manja, komanso atafika ku ofesi yawo anapeza kuti yatsekedwa.
Pakadali pano, iwo ati adziwitsa apolisi za nkhaniyi omwe ayambapo kafukufuku wawo kuti agwire a Lumbe.